Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

Ndime za yesu

Ndikufuna ndikuuzeni za Mpulumutsi wathu, Yesu. Iye ndiye amene anatifera ife pa mtanda chifukwa cha chikondi chake chachikulu. Ndi Mwana wokondedwa wa Mulungu, ndipo kudzera mwa Iye, tili ndi moyo wosatha. Taganizirani zimenezo, moyo wosatha chifukwa cha chikondi chake!

Yesu ndi Mfumu ya mafumu, Ambuye wa ambuye. Anavutika chifukwa cha machimo athu. Amafuna kuti mumuyandikire tsiku lililonse, kuti mumudziwe bwino, ndipo kuti mulankhule naye ngati mmene mungachitire ndi mnzanu wapamtima. Kodi mukuona chikondi chake chachikulu chimenecho?

Amakukondani kwambiri moti anasankha kufera inu. Monga momwe lemba la Luka 19:10 limati, “Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayika.” Tangoganizani, anabwera kudzakufunani inu!

Kudzera mwa Yesu yekha, tingapeze chipulumutso ndi moyo wosatha, ndikutuluka muukapolo wa dziko lapansi lino. Lemba la Machitidwe 4:12 limati, “Ndipo mulibe chipulumutso mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo, lopatsidwa kwa anthu, limene tingapulumutsidwe nalo.” Palibe njira ina, Yesu ndiye njira yekha.


Masalimo 56:3-4

Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu.

Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:11

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:39

Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 16:33

Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 55:16-17

Koma ine ndidzafuulira kwa Mulungu; ndipo Yehova adzandipulumutsa.

Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula, ndipo adzamva mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 20:13

Muimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Nahumu 1:7

Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:10

Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:18

Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 15:2

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:5

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:6-7

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1-2

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 63:3-4

Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.

Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 9:38

Koma iye anati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo anamgwadira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 4:17-18

Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.

Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 126:5-6

Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.

Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:1-2

Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.

Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:1

Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:7-8

Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu, usikunso impso zanga zindilangiza.

Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:10

ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:25-26

Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu.

Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha: Mundiphunzitse malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:38-39

Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,

ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:9-10

Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja;

kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 32:7-8

Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena kutenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asiriya ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe achuluka koposa okhala naye;

pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 100:4

Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 33:27

Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 57:1

Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:1-2

Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.

Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:20

Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:1

Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 63:7-8

Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 150:6

Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:1

Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 10:21

Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 147:1

Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondwetsa ichi, chilemekezo chiyenera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:12

Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 2:2

Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:3

ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 7:22

Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:19

Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 12:9-10

Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

Chifukwa chake ndisangalala m'mafooko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, chifukwa cha Khristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 16:24-25

Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'chipinda cha m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo.

Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:15

Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:16-18

Kondwerani nthawi zonse;

Pempherani kosaleka;

M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:1

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:24

Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 61:1-3

Imvani mfuu wanga, Mulungu; mverani pemphero langa.

Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.

Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 66:1-2

Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi.

Imbirani ulemerero wa dzina lake; pomlemekeza mumchitire ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:26

Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:15

Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:7-8

Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazika, wokhulupirira Yehova.

Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 116:1-2

Ndimkonda, popeza Yehova amamva mau anga ndi kupemba kwanga.

Popeza amanditcherera khutu lake, chifukwa chake ndidzaitanira Iye masiku anga onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:1-2

M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova.

Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:7-10

Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?

Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.

Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja;

kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 25:1

Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 29:11

Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 3:22-23

Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,

chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.

Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 84:11

Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:1-2

Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?

Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:3-5

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;

ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:9-10

Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso;

ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:8-9

Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:13-14

Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani!

Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wopulumutsa! Lero ndikufuulirani ndipo ndikuyang'ana nkhope yanu kuti ndikupatseni ulemerero ndi ulemu. Ulemerero ndi ulemu wonse ndi wanu chifukwa cha nsembe yanu yotipulumutsira ife ndi mwazi wanu wopatulika wokhetsedwa pa mtanda wa pa Gologota. Zikomo chifukwa cha pangano latsopano, lomwe limandilola kulowa pamaso pa mpando wachifundo. Munatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima, Yesu, Mwana wa Mulungu, mkhalapakati pakati pa Mulungu ndi anthu. Zikomo chifukwa chodzipereka nokha chifukwa cha chikondi chanu pa anthu, mukulipira mtengo wapatali chifukwa cha machimo athu. Mawu anu amati: "Mwa Iye tili ndi chiwombolo mwa mwazi wake, ndicho chikhululukiro cha machimo, monga mwa chuma cha chisomo chake." Zikomo chifukwa munavulala chifukwa cha kupanduka kwanga, munaphwanyidwa chifukwa cha machimo anga, ndipo chilango cha mtendere wanga chinali pa Inu. Ulemerero ndi ulemu wonse ndi wanu. M'dzina la Yesu. Ameni!