Lero ndikufuna ndikukumbutse kuti Mulungu amakupatsa mphamvu zokumana ndi vuto lililonse lovuta. Nthawi zambiri timaganiza kuti mavuto akabwera sitikonzeka kulimbana nawo, koma ukunama, Mulungu nthawi zonse amatikonzekeretsa. Mawu ake amati Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha, koma wa mphamvu, chikondi ndi kudziletsa. Choncho limbika mtima, Mulungu ali nawe, akulimbana nkhondo zako zonse.
Gwiritsa ntchito zipangizo zimene Mulungu anakupatsa kudzera m'mawu ake ndi mzimu wake woyera. Khala wolimba mtima, pita patsogolo molimba mtima komanso modzidalira. “Limbikani mtima, mukhale amphamvu, nonsenu inu akuyembekezera Yehova.” (Masalimo 31:24) Choncho limbika mtima, Mulungu sanama.
Mulungu ndiye mphamvu yako, ndiye wokulanditsa wako, ndiye mthandizi wako, ndiye chishango chako, ndiye pothawirapo pako, khulupirira Atate wako wakumwamba, zonse zidzakhala bwino. “Mulungu ndiye amene amandipatsa mphamvu; Mulungu ndiye amene anwongola njira yanga.” (2 Samueli 22:33)
Iye amene akadakomoka, bwenzi lake ayenera kumchitira chifundo; angaleke kuopa Wamphamvuyonse.
Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.
Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.
Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.
Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.
Ndipo wina akamlaka mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha m'khosi zitatu sichiduka msanga.
Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;
Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.
Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke analakika.
Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.
ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.
Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga; ngakhale kupita ndi mwamuna waukali;
kuti ungaphunzire mayendedwe ake, ndi kutengera moyo wako msampha.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.
Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo m'imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.
Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.
Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza chiyani? Adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.
Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.
Ndipo Yonatani anamlumbiritsa Davide kachiwiri, chifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.
Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;
ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine.
nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,
chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;
kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;
kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.
Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?
Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.
Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane, tsamwali wanga, wodziwana nane.
Tinapangirana upo wokoma, tinaperekeza khamu la anthu popita kunyumba ya Mulungu.
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.
Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.
Ndipo kunali m'mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m'nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Saulo munali mkondo.
Ndipo Saulo anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake.
Ndipo Saulo anaopa Davide chifukwa Yehova anali naye, koma adamchokera Saulo.
Chifukwa chake Saulo anamchotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wake wa anthu chikwi chimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kutuluka ndi kubwera nao.
Ndipo Davide anakhala wochenjera m'mayendedwe ake onse; ndipo Yehova anali naye.
Ndipo pamene Saulo anaona kuti analikukhala wochenjera ndithu anamuopa.
Koma Aisraele onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kutuluka ndi kulowa nao.
Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.
Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani m'Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?
Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Saulo kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adriyele Mmehola kukhala mkazi wake.
Ndipo Saulo anamtenga tsiku lomwelo, osamlolanso apite kwao kwa atate wake.
Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anakonda Davide; ndipo pakumva Saulo, anakondwera nako.
Nati Saulo, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Chifukwa chake Saulo ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kachiwiri.
Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu.
Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.
Ndipo anyamata a Saulo anamuuza, kuti, Anatero Davide.
Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.
Ndipo pamene anyamata ake anauza Davide mau awa, kudamkomera Davide kukhala mkamwini wa mfumu.
Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ake, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Saulo anampatsa Mikala mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.
Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide.
Saulo nayamba kumuopa Davide kopambana; ndi Saulo anali mdani wa Davide masiku onse.
Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.
Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,
kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko,
ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;
pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani,
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamanga chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe.
Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;
momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.
Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.
kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachita manyazi ndi unyolo wanga;
komatu pokhala m'Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza.
(Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri m'Efeso, uzindikira iwe bwino.
Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.
Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa.
Pakuti ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.
Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.
Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.
Pakutinso thupi silikhala chiwalo chimodzi, koma zambiri.
Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;
ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
Koma inu simunaphunzira Khristu chotero,
ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu;
kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo;
koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,
nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.
Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.
Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire,
ndiponso musampatse malo mdierekezi.
Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.
Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.
ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.