Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

115 Mau a Mulungu Oteteza Nyumba

Mulungu wandiyang'anira kuyambira ndili m'mimba mwa amayi anga, wanditeteza ku zoipa zonse, wandibisira ku ziwembu za mdani. Ndaona dzanja lake lamphamvu m'moyo wanga, ndipo ndikudziwa kuti ndine cholengedwa chake chamtengo wapatali.

Tsiku lililonse ndimalidza Mulungu chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi zabwino zake zosawerengeka. Ndimalimbikitsidwa ndi Mawu ake opatulika, ndipo ndimapeza mtendere mwa Iye. Ngakhale pakati pa mavuto, ndimadziwa kuti Mzimu Woyera ali nane, akundipatsa chitetezo ndi mphamvu.

Palibe chodetsa nkhawa chifukwa ndikudziwa kuti ndili m'manja mwa Wamphamvuyonse. Mulungu wanga, Mpulumutsi wanga, amanditeteza nthawi zonse. Mwa Iye ndimapeza chimwemwe chenicheni ndi mtendere wosatha.

Mphamvu ya Mulungu imandimasula ku ukapolo wa uchimo ndi mantha. Ndimapembedza mwaufulu, wodzazidwa ndi chikondi chake. Ndimadziwa kuti Mulungu amasamalira moyo wanga, akundipatsa mpumulo umene ndimaufuna.


Masalimo 127:1

Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mudzi Yehova, mlonda adikira chabe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:1-2

Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.

palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.

Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse.

Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala.

Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.

Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.

Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.

Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.

Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:33

Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:11

Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 32:18

Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:7-8

Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako.

Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 32:7

Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 6:6-7

Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu;

ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 12:13

Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 31:6

Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:7

Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:6

Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:17

Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:26

Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:1

Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 4:8

Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 14:14

Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:20

Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:6

Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:7

Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:114

Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 46:4

ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:30

Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:5-6

Sudzaopa choopsa cha usiku, kapena muvi wopita usana;

kapena mliri woyenda mumdima, kapena chionongeko chakuthera usana.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:2

Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 59:16

Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu; inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa, pakuti Inu mwakhala msanje wanga, ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:10

Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:7

Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazika, wokhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 28:15

Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 4:18

Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:2

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 127:3

Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 18:20

Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 3:3

Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:18

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:5-6

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:9

Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso;

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:6-7

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:22

Koma Yehova wakhala msanje wanga; ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:1-2

Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?

Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:4

Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:21

Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:1

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:7-8

Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;

pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3

Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 125:1-2

Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.

Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:3

Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:14

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:2

Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:4

Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:19

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:5

Munandizinga kumbuyo ndi kumaso, nimunaika dzanja lanu pa ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:29

Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:14

Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 50:20

Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:33

Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:24

Wakuitana inu ali wokhulupirika, amenenso adzachichita.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 11:1

Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 40:11

Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:23

Kuopa Yehova kupatsa moyo; wokhala nako adzakhala wokhuta; zoipa sizidzamgwera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 58:11

ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:10

Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 16:11

Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake; funani nkhope yake nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:29-31

Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu:

Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;

komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.

Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:14

Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:7

M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi chitonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; chifukwa chake iwo adzakhala nacho m'dziko mwao cholowa chowirikiza, adzakhala nacho chikondwerero chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:1

Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 32:8

Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 32:2

Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:18

Munditsegulire maso, kuti ndipenye zodabwitsa za m'chilamulo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:3

Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:73

Manja anu anandilenga nandiumba; mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:147

Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:8

Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 48:14

Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:16

Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:6-7

Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha.

Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazika, wokhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:29

Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 28:20

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:19

Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:24

Ukagona, sudzachita mantha; udzagona tulo tokondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:142

Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:6

Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:26

Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:8

Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 116:7

Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako; pakuti Yehova anakuchitira chokoma.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 5:14-15

Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera;

ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 35:27

Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa, ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:134

Mundiombole kunsautso ya munthu: Ndipo ndidzasamalira malangizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 49:25

Koma atero Yehova, Ngakhale am'nsinga a wamphamvu adzalandidwa, ndi chofunkha cha woopsa chidzapulumutsidwa; pakuti Ine ndidzakangana naye amene akangana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 147:3

Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:9

Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 29:15

Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:5-6

M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.

Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:20-21

Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.

Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 24:3-4

Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa.

Ndinapita pa munda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru.

Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka.

Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo.

Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona,

ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.

Kudziwa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:5

Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 10:12

Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima, ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:24

Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:5-8

Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja.

Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku.

Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako.

Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:6-7

Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga wokondedwa, zikomo chifukwa ndinu thanthwe langa lolimba, linga langa, chiyembekezo changa ndi mpulumutsi wanga, amene amandipatsa chitetezo ndi mtendere mumtima mwanga, amene amandiwongolera kuchoka mu ulemerero kupita mu ulemerero wina. M'dzina lamphamvu la Yesu, Ambuye ndimakukwezani ndi kukudalitsani, chifukwa mwanditeteza kuyambira ndili mwana. Lero ndikupempherani Mulungu wanga, kuti munditeteze ndisanayambe tsiku. Ndinu chishango changa ndi mphamvu yanga ndipo pansi pa mapiko anu ndimapeza pothawirapo. Chotsani choipa kutali ndi ine, nditetezeni ku mavuto kulikonse kumene ndili, ngakhale ndili kuti ndikudziwa kuti mudzanditeteza, amene amandimenyera nkhondo ndi Mzimu wanu Woyera ndipo udzandipatsa nzeru zoyendera komwe mapazi anga sadzaterereka. Chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu zimandizungulira ndipo mtima wanga sudzachita mantha ndi nkhani zoipa, chikhulupiriko changa chili mwa inu, Mulungu wa kumwamba ndipo ndikukuthokozani chifukwa chonditeteza ine ndi banja langa, sungani ana anga, makolo anga, abale anga, azakhali anga ndi abwenzi anga m'manja mwanu, tumizani angelo anu kumalo oyenera okonzeka kuchitapo kanthu chifukwa cha iwo ndipo musalole choipa kuwavulaza, awasunge ku mayesero onse ndi kwa iwo amene akufuna kuwononga zikhulupiriro zawo. Mawu anu amati: “Dzikankhireni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti akukwezeni nthawi yake ikafika; mutayire nkhawa zanu zonse pa iye, pakuti iye amasamalira inu.” Ndikulengeza kuti chikhulupiriko changa ndi chidaliro changa zili zolimba pa thanthwe lomwe ndi Khristu. M'dzina la Yesu. Ameni.