Ndikudziwa kuti zinthu zimakhala zovuta munthu wamtima wako akamwalira. Ukumva chisoni chachikulu, ndipo izi ndizachibadwa. Koma usalole kuti chisonichi chikulemere kwambiri. Kumbukira kuti Mzimu Woyera, Mtonthozi wathu, ali nafe. Adzakutonthoza ndi kukupatsa mphamvu kuti upirire nthawi yovutayi.
Monga wokhulupirira, tikudziwa kuti tikachoka padziko lapansi lino, tipita kwabwino kwambiri kwa Ambuye Yesu Khristu. Anthu athu amatipatsa, koma tiyenera kukumbukira kuti ali bwino kuposa ife. Kondwera podziwa kuti miyoyo yawo yapulumutsidwa.
Tinalengedwera Mulungu. Mawu ake amatiuza kuti ngati tili ndi moyo, tili ndi moyo wa Ambuye, ndipo ngati timwalira, timwalira wa Ambuye. Kaya tili ndi moyo kapena tamwalira, ndife a Ambuye. Funa chitonthozo kwa Mulungu, ndipo upumule mwa Iye. Khulupirira kuti Mulungu ali nawe ndipo akufuna kukulimbitsa ndi kutonthoza mtima wako. Ingomulola Mulungu agwire ntchito m'moyo wako.
Yohane 11:25: Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka kwa akufa, ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale atamwalira, adzakhala ndi moyo.”
Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.
Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.
Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,
Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'chikondi cha mulungu ndi m'chipiriro cha Khristu.
Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,
Koma pamene kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidanoneka,
zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine.
Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;
pakuti Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndinatuluka kwa Atate.
Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.
Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.
Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.
Pamene ndinati, Litereka phazi langa, chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.
Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,
ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,
chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako;
motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.
Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.
Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.
Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.
ndi kuchitira chifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.
Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.
ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.
Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera,
koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho,
tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),
koma monga kulembedwa, Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva, nisizinalowa mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.
Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.
Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Yehova wa moyo wanga.
Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima; m'mwemo aona nkhope yake mokondwera; ndipo ambwezera munthu chilungamo chake.
Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka.
ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.
kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,
mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera,
ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Iye amene sanatimana Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha.
Natikwatula kwa otisautsa; pakuti chifundo chake nchosatha.
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,
sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;
sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi;
chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.
Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;
Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.