1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako. 2 Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. 3 Koma Ine ndidzaumitsa mtima wake wa Farao, ndipo ndidzachulukitsa zizindikiro ndi zozizwa zanga m'dziko la Ejipito. 4 Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo aakulu. 5 Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao. 6 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita. 7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao. Mose ndi amatsenga8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti, 9 Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka. 10 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka. 11 Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao. 12 Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao. 13 Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova. Chozizwitsa choyamba: Madzi asanduka mwazi14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite. 15 Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako. 16 Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m'chipululu; koma, taona, sunamvere ndi pano. 17 Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m'mtsinje ndi ndodo ili m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi. 18 Ndi nsomba zili m'mtsinje zidzafa, ndi mtsinje idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m'mtsinjemo. 19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pamadzi a mu Ejipito, pa mitsinje yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala. 20 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'mtsinjemo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m'mtsinjemo anasanduka mwazi. 21 Ndi nsomba za m'mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito. 22 Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova. 23 Ndipo Farao anatembenuka, nalowa m'nyumba yake, osasamalira ichi chomwe mumtima mwake. 24 Koma Aejipito onse anakumba m'mphepete mwa mtsinje kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo. 25 Ndipo anafikira masiku asanu ndi awiri atapanda mtsinje Yehova. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi