Eksodo 7:21 - Buku Lopatulika21 Ndi nsomba za m'mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Nsomba zonse zamumtsinjemo zidafa, ndipo kununkha kwake kwa madziwo kunali kwakuti Aejipito sadathenso kuŵamwa. Ndipo munali magazi okhaokha m'dziko lonse la Ejipito. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto. Onani mutuwo |