Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 7:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'mtsinjemo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m'mtsinjemo anasanduka mwazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m'nyanjamo anasanduka mwazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Motero Mose ndi Aroni adachita monga momwe Chauta adaŵalamulira. Aroni adasamula ndodo yake namenya madzi amumtsinje pamaso pa Farao ndi nduna zake, ndipo madzi onsewo adasanduka magazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova analamulira. Anakweza ndodo yake pamaso pa Farao ndi akuluakulu ake ndipo anamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:20
14 Mawu Ofanana  

Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.


Anasanduliza madzi ao akhale mwazi, naphanso nsomba zao.


Nasanduliza nyanja yao mwazi, ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa.


Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kumtsinje ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku mtsinjewo adzasanduka mwazi pamtunda.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka.


Ndi nsomba za m'mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito.


Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita.


Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje? Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi, kapena ukali wanu panyanja, kuti munayenda pa akavalo anu, pa magaleta anu a chipulumutso?


Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto linaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa