Eksodo 7:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pamadzi a mu Ejipito, pa mitsinje yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pa madzi a m'Ejipito, pa nyanja yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Chauta adalamulanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, uilozetse ku madzi onse mu Ejipito muno, monga mitsinje, ngalande ndiponso zithaphwi ndi maiŵe omwe. Madziwo adzasanduka magazi, ndipo m'dziko monsemo mudzakhala magazi okhaokha, ngakhale m'zotungira madzi zomwe, zamitengo ndi zamiyala.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.” Onani mutuwo |