Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 7:19 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pamadzi a mu Ejipito, pa mitsinje yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pa madzi a m'Ejipito, pa nyanja yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Chauta adalamulanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, uilozetse ku madzi onse mu Ejipito muno, monga mitsinje, ngalande ndiponso zithaphwi ndi maiŵe omwe. Madziwo adzasanduka magazi, ndipo m'dziko monsemo mudzakhala magazi okhaokha, ngakhale m'zotungira madzi zomwe, zamitengo ndi zamiyala.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:19
15 Mawu Ofanana  

Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.


Elisa anawuza Gehazi kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga ndodo yanga mʼdzanja lako ndipo thamanga. Ngati ukumana ndi munthu wina aliyense, usamupatse moni, ndipo ngati wina akupatsa moni, usayankhe. Ukagoneke ndodo yanga pa nkhope ya mwanayo.”


Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Igupto kuti dzombe lidze pa dziko la Igupto ndi kuwononga chilichonse chimene chikumera mʼminda ndi chilichonse chimene chinatsala pa nthawi ya matalala.”


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasulira dzanja lako kumwamba kuti kukhale mdima umene udzaphimba dziko lonse la Igupto, mdima wandiweyani.”


Nyamula ndodo yako ndi kutambasula dzanja lako kuloza ku nyanja, kugawa madzi kuti Aisraeli awoloke powuma.


Kenaka Mose anatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo Yehova pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kummawa imene inawomba usiku wonse anabweza madzi ndi kuwumitsa nyanja ija. Choncho nyanja ija inagawanika.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasula dzanja lako pa nyanja kuti madzi amize Aigupto ndi magaleta awo ndi okwera pa akavalo.”


Koma ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwiri izi kapena kukumvera, ukatunge madzi a mu mtsinje wa Nailo ndi kuwathira pa mtunda powuma ndipo madziwo adzasanduka magazi.”


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti akweze ndodo yake ndi kumenya fumbi la pa nthaka, ndipo fumbilo lidzasanduka nsabwe pa dziko lonse la Igupto.”


Mose anasiyana ndi Farao natuluka mu mzindawo. Iye anakweza manja ake kwa Yehova. Mabingu ndi matalala zinaleka, ndipo mvula inalekeratu kugwa mʼdzikolo.


Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi, ndipo anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzatheratu mphamvu.


Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake; watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha Mapiri akugwedezeka, ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala. Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke, dzanja lake likanali chitambasulire;


Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje? Kodi munakalipira timitsinje? Kodi munapsera mtima nyanja pamene munakwera pa akavalo anu ndiponso magaleta anu achipulumutso?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa