Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 7:21 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

21 Ndi nsomba za m'mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Nsomba zonse zamumtsinjemo zidafa, ndipo kununkha kwake kwa madziwo kunali kwakuti Aejipito sadathenso kuŵamwa. Ndipo munali magazi okhaokha m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:21
7 Mawu Ofanana  

Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi, kuchititsa kuti nsomba zawo zife.


Nsomba za mu Nailo zidzafa, mtsinje udzanunkha ndipo Aigupto sadzatha kumwa madzi ake.’ ”


Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova analamulira. Anakweza ndodo yake pamaso pa Farao ndi akuluakulu ake ndipo anamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi.


Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu.


Aigupto anawunjika achulewo milumilu ndipo dziko linanunkha.


Asodzi adzabuwula ndi kudandaula, onse amene amaponya mbedza mu Nailo; onse amene amaponya makoka mʼmadzi adzalira.


Gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zonse zamoyo za mʼnyanja, linafa, ndipo gawo limodzi la sitima za pamadzi linawonongedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa