Eksodo 7:17 - Buku Lopatulika17 Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m'mtsinje ndi ndodo ili m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo ili m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Zimene Chauta akunena ndi izi, akuti ‘Poona zimene ndichite, udzadziŵa kuti Ine ndinedi Chauta. Taona, ndidzamenya madzi a mu mtsinjewu ndi ndodo ili m'manja mwangayi, ndipo madzi onseŵa adzasanduka magazi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: Onani mutuwo |
ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama zakuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.