Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 7:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamenepo nkuti Mose ali wa zaka 80 ndipo Aroni wa zaka 83, pa nthaŵi imene ankalankhula ndi Farao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mose anali ndi zaka 80, ndipo Aaroni anali ndi zaka 83 pamene anakayankhula kwa Farao.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:7
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita padziko lonse la Ejipito.


Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.


Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti,


Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori.


Koma pamene zaka zake zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwake kuzonda abale ake ana a Israele.


Ndipo zitapita zaka makumi anai, anamuonekera mngelo m'chipululu cha Sinai, m'lawi la moto wa m'chitsamba.


Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu; zovala zanu sizinathe pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinathe pa phazi lanu.


nati nao, Ndine munthu wa zaka zana ndi makumi awiri lero lino; sindikhozanso kutuluka ndi kulowa; ndipo Yehova anati kwa ine, Sudzaoloka Yordani uyu.


Ndipo zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachite mdima, ndi mphamvu yake siidaleke.


Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aejipito, monga ndinachita pakati pake; ndipo nditatero ndinakutulutsani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa