Chilango cha Mulungu pa amitundu ozinga Israele1 Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi. 2 Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali mu Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali mu Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma. 3 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo; 4 koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi. 5 Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova. 6 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu; 7 koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu; 8 ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova. 9 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale; 10 koma ndidzatumiza moto pa linga la Tiro, ndipo udzanyeketsa nyumba zake zachifumu. 11 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire; 12 koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira. 13 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao; 14 koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu; 15 ndipo mfumu yao idzalowa kundende, iyo ndi akalonga ake pamodzi, ati Yehova. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi