Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 1:7 - Buku Lopatulika

7 koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono Ine ndidzaponya moto pa makoma ozinga Gaza, udzatentha malinga ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 ndidzatumiza moto pa makoma a Gaza umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 1:7
17 Mawu Ofanana  

Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ake, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mzinda walinga.


popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga mizinda m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.


Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza.


Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'chidikha chao; udzadzicheka masiku angati?


Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto mu Ejipito, naonongeka onse akumthandiza.


Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m'zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu;


ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.


Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekeroni adzazulidwa.


Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.


Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa