Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 1:8 - Buku Lopatulika

8 ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 ndipo ndidzalikha okhala m'Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu m'Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ndidzaonongeratu onse okhala ku Asidodi, kudzanso iye amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni. Ndidzakantha mzinda wa Ekeroni ndi dzanja langa, ndipo Afilisti onse otsalira adzaonongeka.” Akuterotu Ambuye Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndidzawononga mfumu ya ku Asidodi komanso amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni. Ndidzalanga Ekroni, mpaka wotsala mwa Afilisti atafa,” akutero Ambuye Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 1:8
17 Mawu Ofanana  

popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga mizinda m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.


Ndikadagonjetsa adani ao msanga, ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.


ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzachotsa seta wako wonse:


Chaka chimene kazembe wa ku Asiriya anafika ku Asidodi, muja Sarigoni mfumu ya Asiriya anamtumiza iye, ndipo iye anamenyana ndi Asidodi, naugonjetsa.


Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza.


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatambasulira Afilisti dzanja langa, ndi kulikha Akereti, ndi kuononga otsalira mphepete mwa nyanja.


Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Filistiya? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu.


koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu;


Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero aakulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.


Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati chiputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.


Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala mu Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti.


Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolide amene Afilisti anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yopalamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekeroni limodzi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa