Amosi 1:9 - Buku Lopatulika9 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Tiro akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adapereka mtundu wathunthu wa anthu ku Edomu, osasunga chipangano chaubale chija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu, osasunga pangano laubale lija, Onani mutuwo |