Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 1:13 - Buku Lopatulika

13 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa Aamoni akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo pofuna kufutuza malire ao, adatumbula akazi apakati ku Giliyadi,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadi nʼcholinga choti akuze malire awo,

Onani mutuwo Koperani




Amosi 1:13
27 Mawu Ofanana  

Natulutsa anthu a m'mzindamo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi mizinda yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kunka ku Yerusalemu.


Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.


Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.


Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.


Ndipo zitatha izi, kunachitika kuti ana a Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.


Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;


Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?


Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.


Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, amene alumikiza munda ndi munda, kufikira padzapanda malo, ndipo inu mudzasiyidwa nokha pakati padziko!


Edomu, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni,


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za chitonzo chao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira.


Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,


Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati cholowa chathu, angakhale Yehova anali komweko;


Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.


Israele, bwerera kunka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo;


Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawavuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lakolako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale laolao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa