Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 26:20 - Buku Lopatulika

Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Potsata mabanja ao ana ena aamuna a Yuda anali aŵa: Sela anali kholo la banja la Asela. Perezi anali kholo la banja la Aperezi. Zera anali kholo la Azera.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Sela, fuko la Asera; kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi; kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera.

Onani mutuwo



Numeri 26:20
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake.


Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili panjira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake.


Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye.


Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.


Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.


Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,


Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.


Ndipo a Asiloni: Asaya woyamba, ndi ana ake.


Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo.


Ndipo mu Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi;


Ana onse a Perezi okhala mu Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu.


Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli.


ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;


mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,


Mwa fuko la Yuda anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri.