Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 11:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo mu Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo m'Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ku Yerusalemu kunkakhalanso ena a fuko la Yuda ndiponso ena a fuko la Benjamini. Zina mwa zidzukulu za Yuda ndi izi: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, onsewo anali ana a Perezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ku Yerusalemu kunkakhalanso anthu ena a mafuko a Yuda ndi Benjamini. Ena mwa zidzukulu za Yuda ndi awa: Ataya, mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalaleli. Onsewa anali ana a Perezi.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 11:4
7 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziphothyolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi.


Awa tsono ndi akulu a dziko okhala mu Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi antchito a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni.


ndi Maaseiya mwana wa Baruki, mwana wa Kolihoze, mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribu, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni.


ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;


mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,


Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa