Nehemiya 11:3 - Buku Lopatulika3 Awa tsono ndi akulu a dziko okhala mu Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi antchito a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomoni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Aisraele wamba ambiri, pamodzi ndi ansembe, Alevi, anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso zidzukulu za atumiki a Solomoni, onsewo ankakhala m'midzi mwao, aliyense m'dera la choloŵa chake. Koma akuluakulu a m'chigawo cha Yuda anali atakhazikika ku Yerusalemu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Aisraeli wamba, ansembe, Alevi, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ndiponso zidzukulu za antchito a Solomoni ankakhala mʼmidzi yawo, aliyense mu dera lake. Koma atsogoleri a chigawo cha Yuda anali atakhazikika mu Yerusalemu. Onani mutuwo |