Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 46:12 - Buku Lopatulika

12 Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndi ana amuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana amuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ana a Yuda anali aŵa: Ere, Onani, Sela, Perezi ndi Zera, (koma Ere ndi Onani adaafera ku Kanani.) Ana a Perezi anali aŵa: Hezironi ndi Hamuli.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ana aamuna a Yuda ndi awa: Eri, Onani, Sela, Perezi ndi Zera. Koma Eri ndi Onani anamwalira mʼdziko la Kanaani. Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 46:12
29 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; chifukwa chake anamutcha dzina lake Yuda; pamenepo analeka kubala.


Koma chimene iye anachita chinali choipa pamaso pa Yehova, ndipo anamupha iyenso.


Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Onani.


Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye.


Koma Eri mwana wake woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye.


Ndi ana aamuna a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari.


Ndi ana aamuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Iyobu, ndi Simironi.


Ana a Israele ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuloni,


Ana a Davide tsono ombadwira ku Hebroni: woyamba Aminoni wa Ahinowamu wa ku Yezireele, wachiwiri Daniele wa Abigaile wa ku Karimele,


Ana a Yuda: Perezi, Hezironi, ndi Karimi, ndi Huri, ndi Sobala.


Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,


Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);


Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.


Ndi a ana a Zera: Yeuwele ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.


Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo.


koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda.


Wa Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu.


Za Yuda ndi izi; ndipo anati, Imvani, Yehova, mau a Yuda, ndipo mumfikitse kwa anthu ake; manja ake amfikire; ndipo mukhale inu thandizo lake pa iwo akumuukira.


Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.


ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m'dzanja lake.


ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa