Genesis 38:14 - Buku Lopatulika14 Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili panjira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili pa njira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Tsono Tamarayo adasintha zovala zake zaumasiye zija navala zina. Adadziphimba kumaso ndi nsalu, nakakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu. Mudzi wa Enaimu unali pa mseu wopita ku Timna. Adaadziŵa kuti pa nthaŵiyo nkuti Sela atakula, komabe Tamara anali asanamloŵe chokolo Sela uja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 iye anavula zovala zake za umasiye, nadziphimba nkhope ndi nsalu kuti asadziwike, ndipo anakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu popita ku Timna. Tamara anachita izi chifukwa anaona kuti ngakhale Selayo anali atakula tsopano, iye sanaperekedwe kuti amulowe chokolo. Onani mutuwo |