Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 11:24 - Buku Lopatulika

24 Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Tsono Petahiya, mwana wa Mesezabele, mmodzi mwa adzukulu a Sera wa m'fuko la Yuda, ankaimirira Aisraele ku bwalo la mfumu ya ku Persiya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Petahiya mwana wa Mesezabeli, mmodzi mwa zidzukulu za Zera mwana wa Yuda ndiye ankayimirira Aisraeli pa bwalo la mfumu ya Perisiya.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 11:24
8 Mawu Ofanana  

Ndipo pambuyo pake anabadwa mbale wake, amene anali ndi chingwe chofiira pamkono pake, dzina lake linatchedwa Zera.


Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.


ndi Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti; koma ana a Davide ndiwo oyamba ku dzanja la mfumu.


Pakuti ntchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde ntchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;


Mesezabele, Zadoki, Yaduwa,


Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.


Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.


ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa