Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 38:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adabalanso mwana wina wamwamuna, namutcha Sela. Pamene Sela ankabadwa, nkuti Yuda ali ku Kezibu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Anaberekanso mwana wina wamwamuna ndipo anamutcha Sela. Ameneyu anabadwa Yuda ali ku Kezibi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 38:5
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake.


Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatse iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo.


Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wake woyamba mkazi, ndipo dzina lake ndilo Tamara.


Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.


Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha.


Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,


Ana aamuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.


Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa