Numeri 2:34 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Iwo adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Adamanga zithando zao pafupi ndi mbendera zao. Choncho adanyamuka ulendo wao aliyense pa banja lake, potsata banja la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Aisraeli anachita zonse zomwe Yehova analamulira Mose. Umo ndi momwe amamangira misasa yawo pamene panali mbendera zawo, ndipo ankasamuka monga mwa mafuko a makolo awo. |
Ndipo ana a Israele amange mahema ao, yense ku chigono chake, ndi yense ku mbendera yake, monga mwa makamu ao.
Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani.
Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira.
Sayang'anira mphulupulu ili mu Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli mu Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.
Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.
Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.
Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.