Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:1 - Buku Lopatulika

1 Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nayi mibadwo ya Aroni ndi Mose pa nthaŵi imene Chauta adalankhula ndi Mose pa phiri la Sinai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Iyi ndi mbiri ya banja la Aaroni ndi Mose pa nthawi yomwe Yehova anayankhula ndi Mose pa phiri la Sinai.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:1
11 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.


Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.


Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;


Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.


Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele mu Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi kuti,


Awa ndi malamulo, amene Yehova analamula Mose, awauze ana a Israele, m'phiri la Sinai.


Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.


Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa