Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 24:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adaona Aisraele ali m'mahema mwao, fuko lililonse pa lokha. Tsono mzimu wa Mulungu udatsika pa iye,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:2
17 Mawu Ofanana  

Pamenepo mzimu wa Mulungu unagwera Azariya mwana wa Odedi,


Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuwa, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera?


Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza, wokoma ngati Yerusalemu, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera.


Ha? Mahema ako ngokoma, Yakobo; zokhalamo zako, Israele!


Simoni Mkanani, ndi Yudasi Iskariote amenenso anampereka Iye.


Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.


Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?


Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.


Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,


Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israele, natuluka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesopotamiya m'dzanja lake; ndi dzanja lake linamgonjetsa Kusani-Risataimu.


Ndipo pamene anafika ku Gibea, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao.


Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso.


Ndipo anapita komweko ku Nayoti mu Rama; ndi mzimu wa Mulungu unamgwera iyenso; ndipo anapitirira, nanenera, mpaka anafika ku Nayoti mu Rama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa