Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 2:34 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Choncho Aisraeli anachita zonse zomwe Yehova analamulira Mose. Umo ndi momwe amamangira misasa yawo pamene panali mbendera zawo, ndipo ankasamuka monga mwa mafuko a makolo awo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

34 Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Iwo adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Adamanga zithando zao pafupi ndi mbendera zao. Choncho adanyamuka ulendo wao aliyense pa banja lake, potsata banja la makolo ao.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 2:34
15 Mawu Ofanana  

Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi, poganizira malamulo anu onse.


Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose.


monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:


Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake.


Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.


Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani.


Umenewu ndiwo unali mndandanda wa kayendedwe ka magulu a Aisraeli pamene ankanyamuka ulendo wawo mʼmagulumagulu.


“Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.”


Koma Alevi sanawawerenge pamodzi ndi Aisraeli enawo monga momwe Yehova analamulira Mose.


“Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo, sanaone chovuta mu Israeli. Yehova Mulungu wawo ali nawo: mfuwu wa mfumu uli pakati pawo.


Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye


Iyi ndi mbiri ya banja la Aaroni ndi Mose pa nthawi yomwe Yehova anayankhula ndi Mose pa phiri la Sinai.


Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa