Masalimo 8:3 - Buku Lopatulika Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake, |
Kodi Mulungu sakhala m'mwamba m'tali? Ndipo penyani kutalika kwake kwa nyenyezi, zili m'talitali.
Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.
Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.
Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.
Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.