Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 111:2 - Buku Lopatulika

2 Ntchito za Yehova nzazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ntchito za Yehova nzazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ntchito za Chauta nzazikulu, onse okondwera nazo amazilingalira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 111:2
28 Mawu Ofanana  

Tamverani ichi, Yobu. Taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu.


Atsekereza mokhomera chizindikiro dzanja la munthu aliyense, kuti anthu onse anawalenga adziwe.


amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.


Wochita zazikulu zosasanthulika, ndi zodabwitsa zosawerengeka.


Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.


Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova.


Wokhala nazo nzeru asamalire izi, ndipo azindikire zachifundo za Yehova.


M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:


Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.


Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.


Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la chitsiru, popeza wopusa alibe mtima?


Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.


Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.


Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?


Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo.


Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;


pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.


ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife okhulupirira, monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba,


Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa