Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 31:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, pa phiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Chauta atatsiriza kulankhula ndi Mose pa phiri la Sinai lija, adampatsa Moseyo miyala iŵiri yaumboni, imene Mulungu mwini anali atalembapo kale.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Yehova atamaliza kuyankhula ndi Mose pa phiri la Sinai, anamupatsa Mose miyala iwiri yaumboni, imene Mulungu analembapo ndi chala chake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 31:18
17 Mawu Ofanana  

Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.


Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.


Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;


Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.


Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.


popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata ya Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.


Ndipo analembera pamagome, monga mwa malembedwe oyamba, mau khumiwo, amene Yehova adanena ndi inu m'phirimo, ali pakati pa moto, tsiku la kusonkhanako; ndipo Yehova anandipatsa awa.


Pamenepo anakufotokozerani chipangano chake, chimene anakulamulirani kuchichita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.


Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.


okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa