Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 31:17 - Buku Lopatulika

17 ndicho chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi ana a Israele; pakuti Yehova analenga kumwamba ndi dziko lapansi m'masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonanso mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 ndicho chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi ana a Israele; pakuti Yehova analenga zam'mwamba ndi dziko lapansi masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonanso mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Chimenechi ndi chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi Aisraele, chakuti Ine Chauta ndidalenga kumwamba ndi dziko lapansi pa masiku asanu ndi limodzi, ndipo ndidapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Tsiku la Sabata lidzakhala chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi Aisraeli chosonyeza kuti Yehova analenga za kumwamba ndi dziko lapansi kwa masiku asanu ndi limodzi ndi kuti pa tsiku lachisanu ndi chiwiri analeka kugwira ntchito napumula.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 31:17
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.


muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?


Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha; Yehova akondwere mu ntchito zake;


chifukwa m'masiku asanu ndi limodzi Yehova adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.


Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.


Chifukwa chake ana a Israele azisunga Sabata, kuchita Sabata mwa mibadwo yao, likhale pangano losatha;


Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;


Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.


Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.


muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa