Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 8:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 8:3
18 Mawu Ofanana  

Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.


“Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba? Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!


Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka? Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?


Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni, ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,


Kumbukirani kutamanda ntchito zake zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo.


Mwezi umasiyanitsa nyengo ndipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera.


Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira.


Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi, mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.


Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu; thambo limalalikira ntchito za manja ake.


Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.


Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu; munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.


Yehova atamaliza kuyankhula ndi Mose pa phiri la Sinai, anamupatsa Mose miyala iwiri yaumboni, imene Mulungu analembapo ndi chala chake.


Amatsenga anati kwa Farao, “Izi wachita ndi Mulungu.” Koma mtima wa Farao unali wowumabe ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananenera.


Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu.


Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula.


Ndipo pamene muyangʼana kumwamba muona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonse zakumwambazo musakopeke kuti muzigwadire ndi kumapembedza zinthu zimene Yehova wapereka kwa anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa