Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana aamuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha.
Masalimo 7:2 - Buku Lopatulika kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti iwo anganding'ambe ngati mkango, ndi kundikadzula popanda wina wondipulumutsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mwina angandikadzule ngati mkango, ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa. |
Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana aamuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha.
Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.
Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.
Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi; akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinachidziwe, ananding'amba osaleka.
Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.
Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.
Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.
Ndi za Gadi anati, Wodala iye amene akuza Gadi; akhala ngati mkango waukazi, namwetula dzanja, ndi pakati pamutu pomwe.
Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku chigwa chokhala ku Beterehobu. Pamenepo anamanganso mzindawo, nakhala m'mwemo.