2 Samueli 14:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana aamuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana amuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Ndiye ine mdzakazi wanu ndinali ndi ana aamuna aŵiri, anawo ankamenyana kuminda. Panalibe wina aliyense woti aŵaleretse, choncho wina adakantha mnzake mpaka kumupha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ine wantchito wanu ndinali ndi ana aamuna awiri. Iwo anayamba kumenyana mʼmunda, ndipo panalibe woti awaleretse. Wina anakantha mnzakeyo mpaka kumupha. Onani mutuwo |
Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.