2 Samueli 14:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Tsono banja lonse landiwukira ine mdzakazi wanu, akunena kuti, ‘Utipatse mwana wako amene adapha mbale wake, kuti ife timuphe chifukwa cha mbale wake amene iye adaphayo.’ Motero anthuwo adzaononganso mloŵachuma. Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika, pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Tsono banja lonse landiwukira ine, wantchito wanu. Iwo akuti, ‘Utipatse mwana amene anakantha mʼbale wakeyo kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mʼbale wake amene anaphedwayo. Ife tidzaphanso mlowamʼmalo.’ Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.” Onani mutuwo |