Koma maso a oipa adzagoma, ndi pothawirapo padzawasowa, ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao.
Masalimo 69:3 - Buku Lopatulika Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwaa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndafooka ndi kulira kwanga, kum'mero kwanga kwauma. M'maso mwada pamene ndikuyembekezera Mulungu wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndafowoka ndikupempha chithandizo; kummero kwanga kwawuma gwaa, mʼmaso mwanga mwada kuyembekezera Mulungu wanga. |
Koma maso a oipa adzagoma, ndi pothawirapo padzawasowa, ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao.
Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.
Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.
Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.
Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.
Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.
Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.
Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.
Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,