Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:28 - Buku Lopatulika

28 Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Yesu adaadziŵa kuti tsopano zonse wakwaniritsa. Tsono kuti zipherezere zimene Malembo adaanena, Iye adati, “Ndili ndi ludzu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Atadziwa kuti zonse zatha tsopano komanso kuti malemba akwaniritsidwe, Yesu anati, “Ine ndili ndi ludzu.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:28
14 Mawu Ofanana  

Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.


Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.


Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!


Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.


Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro.


amene anaonekera mu ulemerero, nanena za kumuka kwake kumene Iye ati adzatsiriza ku Yerusalemu.


Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.


Ine ndalemekeza Inu padziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.


Pamenepo Yesu, podziwa zonse zilinkudza pa Iye, anatuluka, nati kwa iwo, Mufuna yani?


Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi.


Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.


Pakuti izi zinachitika, kuti lembo likwaniridwe, Fupa la Iye silidzathyoledwa.


Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.


Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za Iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa