Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 2:11 - Buku Lopatulika

11 Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasula kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Maso anga atopa nkulira, moyo wanga wazunzika zedi, Mumtima mwanga mwadzaza chisoni, chifukwa choti anthu anga aonongeka, ana ndi makanda omwe akukomoka m'miseu yamumzinda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Maso anga atopa ndi kulira, ndazunzika mʼmoyo mwanga, mtima wanga wadzaza ndi chisoni chifukwa anthu anga akuwonongeka, chifukwa ana ndi makanda akukomoka mʼmisewu ya mu mzinda.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:11
26 Mawu Ofanana  

Eni mauta ake andizinga, ang'amba impso zanga, osazileka; natsanulira pansi ndulu yanga.


M'kati mwanga mupweteka mosapuma, masiku a mazunzo andidzera.


Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu, ndikuti, Mudzanditonthoza liti?


Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine. Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mavuto.


Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa, ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga.


Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni; lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa.


Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwaa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.


Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.


Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.


Ana ako aamuna akomoka; agona pamutu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.


Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa chanji muchitira miyoyo yanu choipa ichi, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.


Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.


Onani, Yehova; pakuti ndavutika, m'kati mwanga mugwedezeka; mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu; kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.


Chifukwa cha ichi mtima wathu ufooka, chifukwa cha izi maso athu achita chimbuuzi;


Chifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.


Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa