Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Adandipatsa ulembe kuti ndidye, ndipo nditamva ludzu, adandipatsa vinyo wosasa kuti ndimwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:21
13 Mawu Ofanana  

Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.


Chifukwa chake Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo chowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kunka ku dziko lonse.


Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.


chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa chivumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.


Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.


Udyo wake unali m'nsalu zake; sunakumbukire chitsiriziro chake; chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza; taonani, Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.


anamwetsa Iye vinyo wosakaniza ndi ndulu; ndipo Iye, m'mene analawa, sanafune kumwa.


Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, natenga chinkhupule, nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye.


Ndipo anampatsa vinyo wosakaniza ndi mure; koma Iye sanamlandire.


Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa.


Ndipo asilikalinso anamnyoza, nadza kwa Iye, nampatsa vinyo wosasa,


kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa