Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:20 - Buku Lopatulika

20 Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Mtima wanga wasweka chifukwa cha zipongwe, ndataya mtima kotheratu. Ndidafunafuna ena ondichitira chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe. Ndidafunafunanso ena ondisangalatsa, koma sindidampeze ndi mmodzi yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mnyozo waswa mtima wanga ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse; ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:20
15 Mawu Ofanana  

Ndamva zambiri zotere; inu nonse ndinu otonthoza mtima mondilemetsa.


Moyo wathu wakhuta ndithu ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu, ndi mnyozo wa odzikuza.


Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.


Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?


Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.


Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wochirikiza; chifukwa chake mkono wangawanga unanditengera chipulumutso, ndi ukali wanga unandichirikiza Ine.


Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.


Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?


Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.


Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.


Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,


kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa