Masalimo 6:5 - Buku Lopatulika Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu; m'mandamo adzakuyamikani ndani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu; m'mandamo adzakuyamikani ndani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu akufa sangathe kukutamandani ku manda. M'dziko la akufa ndani angathe kukuyamikani? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda? |
Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova; ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.
M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje? Ngati fumbi lidzayamika Inu? Ngati lidzalalikira choonadi chanu?
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.