Masalimo 57:4 - Buku Lopatulika Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimagona pakati pa anthu olusa amene ali ngati mikango. Mano ao ali ngati mikondo ndi mivi, lilime lao lili ngati lupanga lakuthwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndili pakati pa mikango, ndagona pakati pa zirombo zolusa; anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi, malilime awo ndi malupanga akuthwa. |
Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.
Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.
Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.
Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.
Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.
Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni; kuti adye osauka kuwachotsa kudziko, ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.
Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.
Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.
koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki.