Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 58:6 - Buku Lopatulika

6 Thyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu, zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Thyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu, zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Inu Mulungu, gululani mano a m'kamwa mwao, phwanyani nsagwada za mikangoyi, Inu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu, Yehova khadzulani mano a mikango!

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 58:6
14 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinathyola nsagwada ya wosalungama, ndi kukwatula chogwidwa kumano kwake.


Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pake? Mano ake aopsa pozungulira pao.


Thyolani mkono wa woipa; ndipo wochimwa, mutsate choipa chake kufikira simuchipezanso china.


Afanana ndi mkango wofuna kumwetula, ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.


Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.


Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.


Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.


Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri la Ziyoni, ndi kuchitunda kwake komwe.


Pakuti, taonani, ndidzatumiza pa inu njoka, mphiri, zosalola kuitanidwa; ndipo zidzakulumani inu, ati Yehova.


Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa