Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
Masalimo 45:3 - Buku Lopatulika Dzimangireni lupanga lanu m'chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dzimangireni lupanga lanu m'chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu ngwazi yolimba mtima, mangirirani lupanga lanu m'chiwuno, mu ulemerero ndi ukulu wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu; mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu. |
Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
Pakuti mfumu akhulupirira Yehova, ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye.
Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.
Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.
Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo, ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira: Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure.
nachititsa pakamwa panga ngati lupanga lakuthwa, mu mthunzi wa dzanja lake wandibisa Ine; wandipanga Ine; muvi wotuulidwa; m'phodo mwake Iye wandisungitsa Ine, nati kwa Ine,
Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)
Pakuti, chifukwa cha ichi Khristu adafera, nakhalanso ndi moyo, kuti Iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo.
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
Koma mutu wa izi tanenazi ndi uwu: Tili naye Mkulu wa ansembe wotere, amene anakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu mu Kumwamba,
kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.
Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.
Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.
ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lotuluka m'kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao.
Ndipo Ehudi anadzisulira lupanga lakuthwa konsekonse utali wake mkono; nalimangirira pansi pa zovala zake pa ntchafu ya kulamanja.