Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.
Masalimo 4:3 - Buku Lopatulika Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo, adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo, adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma tsono mudziŵe kuti Chauta wadzipatulira Iye yemwe anthu olungama. Chauta amamva ndikamuitana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika; Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana. |
Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.
Pakamwa panga padzanena zanzeru; ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso.
Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.
Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake; pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.
Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.
Pakuti chidziwika ndi chiyani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?
Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;