16 Pakuti chidziwika ndi chiyani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?
16 Pakuti chidziwika ndi chiyani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?
16 Nanga zidzadziŵika bwanji kuti mwandikomera mtima ine pamodzi ndi anthu anu? Kodi si chifukwa chakuti mumapita nafe, ine pamodzi ndi anthu anu, kuti tizikhala osiyana ndi anthu ena onse a pa dziko lapansi?”
Ndiponso mtundu uti wa padziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?
Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitike zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.
Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu.
ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.
Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?