Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.
Masalimo 3:5 - Buku Lopatulika Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo; ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo; ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimagona ndipo ndimapeza tulo. Ndimadzukanso m'maŵa pakuti Chauta amanditchinjiriza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza. |
Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.
Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.
Ndipo pamene Herode anati amtulutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhala pakhomo anadikira ndende.