Machitidwe a Atumwi 12:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo pamene Herode anati amtulutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhala pakhomo anadikira ndende. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo pamene Herode anati amtulutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhala pakhomo anadikira ndende. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Usiku woti m'maŵa mwake Herode azenga mlandu wake, Petro adaagona pakati pa asilikali aŵiri. Anali womangidwa ndi maunyolo aŵiri, ndipo pakhomo pa ndende panali alonda ena. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Usiku woti mmawa mwake Herode amuzenga mlandu, Petro amagona pakati pa asilikali awiri, atamangidwa maunyolo awiri, ndiponso alonda atayima pa khomo. Onani mutuwo |