Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya. Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.
Masalimo 2:6 - Buku Lopatulika Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzati, “Ine ndakhazika kale mfumu yanga, ili pa phiri langa loyera la Ziyoni.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” |
Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya. Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.
Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kuiika; ndidzabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kuioka paphiri lalitali lothuvuka;
Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.
Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwa Mpingo
Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,
Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.